Akufuna kundigulitsira malo

Ndine mzimayi wakuno kwa mtsiliza, ankolo anga anandisiyira malo ndipo atamwalira akazi awo akufuna kundilanda malowo ponena kuti ndi awo, titapita ku court chaka chatha anagamula kuti malo ndi awo poti alindimapepala. Koma malowa ndi anga ndipo mene amandipatsa ankolowo panali mamfumu awiri omwe amayimira ngati mboni. Mundithandize poti chigamulocho sichinandisangalatse ndipo athuwo akufuna kugulitsa malawo.