Ndine Mzimayi wakwa Tsiliza ku Mtandire. Ndakhala ndikugwira tchito yapakhomo kwazaka 5 kuchokera 2009, ku Gulliver, atasamukira ku 25 abwana anga anandiuza kuti ndiyime kaye poti kumatalika kuchoka ku Mtandire kukafika ku 25 sector C. Koma ananditsimikizira kuti akasamuka azandiuza kuti ndizayambireso. Atasamukira ku 47 mu 2017 anandiyimibira kuti ndikayambireso ndipo ndinakayamba. Patatha miyezi itatu kuona kuti palibe zokambirana zilizonse ndinawafusa kuti kodi gwirizano wake ukhala wotani, ndikhala ngati ndayambiraso kapena ndikupitiliza, ndipo anandiuza kuti ndikhala ngati ndayambiraso, koma titakambirana tinagwirizana kuti azandiganizirako. Patatha mwezi umodzi ndinaona kuti tchito imandikulira nde ndinatsazika. Abwana anga anandipatsa 25 000 salary yanga ya mwezi umenewo, ndikundiuza kuti ndizabwere pa 15 azandiganizire malinga ndi momwe tinagwirizirana. Nditabwera anandilalatira kundibweza, ndikundiuza kuti ndizayimbe phone, koma nditakayimba phone tsiku lina anandilalatiraso kundiuza kuti ndisadzaimbeso phone komaso ndisazapiteso kunyumba kwawo ndipo ndalamayo sadzandipatsaso. Chonde ndithandizeni.
11
Jul