Ine kuno kwa mfumu Chigoneka ku Mtandire mu Mzinda wa Lilongwe. Ndimagwira ntchito ngati garden boy ku Area 18 B. Koma zomwe akundipanga a bwana anga sizikundisangalatsa. Iwo akumandigwiritsanso ntchito ku poloti yawo yoperekera matope koma malipiro sanandionjezere. Ndimalandira K20,000 pa mwezi koma ndi ntchito yomwe andionjezerayi malipirowa sakukwanira, ntchito yachuluka. Chonde ndithandizeni kuti pamenepa ndipange bwanji. Zikomo
08
Sep