Ndine mtsikana wa zaka 15 kuno kwa Mtsiliza mu mzinda wa Lilongwe. Amayi anga akundikakamiza kukwatiwa. Iwo akundithamangitsa pakhomo pawo ponena kuti ndakula azikandiveka mwamuna amene andikwatire. Koma ine ndinawauza kuti sindikufuna banja koma sukulu. Pakusamvetsetsa chomwe ine ndikufuna mayi anga amandimenya nkundiuza kuti pakhomo pawo sakundifuna koma ndikwatiwe. Iwo akuti atopa kundidyetsa, pano ndakula ndikwatiwe kuti azikandidyetsa mwamuna wanga. Chonde ndithandizeni, ine ndikufuna kuphunzira kaye, banja ayi sindikakwanitsa.
08
Sep