Amuna anga akumandizuza kamba ka mkazi wachiwiri

Ine kuno Kwa mfumu a kanyemba mu Mtandire ndili ndi dandaulo lomwe likufuna thandizo lanu. Amuna anga anakwatira akazi achiwiri ndipo akumandizuza, kundimenya, kundibisira zakudya, tikunena pano anandilanda katundu ndipo khawa zanga ndizakuti akhoza kundigulitsira malo.