Ndine mtsikana wa zaka 15 mmudzi mwa Chigoneka ku Mtandire mu Mzinda wa Lilongwe. Ndinatengeka ndi mzanga yemwe ankakhala ndi mtiskana okulirapo. Mtsikanayu amabweretsa amuna usiku kuti tizigona nawo koma malipiro amatenga ndiyeyo. Iye amati ndalamazo akumalipira malo ogona komanso kutigulira zakudya tsiku ndi tsiku. Mkulu wathuyu amati akabweretsa amuna timagona nawo kwa maola osachepera awiri. Ndipo mchitidwewu umachitika usiku uliwonse komanso popanda chitetezo kapena kuti Chishango. Izi zinakhala zikuchitika kwa miyezi iwiri kenaka ndinayamba kumva kupweteka m’mimba komanso ululu kumaliseche. Patapita masiku kumaliseche kuja kunayamba kutupa mpaka ndimalephera kukhala ngakhalenso kuyenda. Zitafika pa mulingo umenewu ndinaganiza zobwerera kwathu ndipo ndinatengeredwa ku chipatala.
21
Aug