Ndine mzimayi wa ana atatu ndipo ndimakhala ku mtandire mu Mzinda wa Lilongwe. Mwamuna wanga amafuna kundidula maliseche ndi cholinga chopangira mankhwala kuti apeze chuma, koma ine ndinakana. Patapita nthawi, anapemphaso mchombo wa mwana wathu wachitatu atangobadwa kumene. Nkhaniyi ine sindinagwirizane nayobe ndipo pachifukwa chimenechi anandithamangitsa mu nyumba yomwe tinamangira limodzi. Ndikunena pano ndikusowa pokhala pamodzi ndi ana. Ndithandizeni.