Ndine m’busa kuno kwa Mtsiliza, mu mzinda wa Lilongwe. Mtsikana wa zaka 15, komanso oyembekezera anandipeza kuti akusowa pokhala. Nditamufunsa bwino bwino iye anati mamuna yemwe anamupatsa pathupi anamuthawa ndipo komwe anapita sikukudziwika, makolo ake sakudziwa komwe ali. Patapita masiku atatu ndikumusungabe, tinazindikira kuti agogo ake akukhala m’dera lathu la Mtsiliza ndipo ndinamtenga kupita naye ku nyumba kwa agogo ake. Koma chondidabwitsa ndi chakuti titafika kunyumbako, agogo ake amtsikanayu sanatilandire ndipo iwo anati sakumufuna mtsikanayo pa nyumba pawo. Nditawafunsa chifukwa chomwe amatithamangitsira iwo anati sakufuna mbava pakhomo pawo. Ine nkhaniyi yandikulira, poona kuti sindingakwanitse kumusunga mtsikana wapathupi pamene mkazi wanga palibe. Ndithandizeni.
29
Aug