Ndimafuna chithandizo cha azing'ono anga pakhani yamaphunziro

Ndine mtsikana wochokera kwa Kaliyeka, Area 22. Ndi masunga azibale anga chifukwa amayi anga anamwalira pamene abambo anga ali moyo koma samadziwika komwe amakhala. Sukulu ndinalekeza Form 4 chifukwa cha mavuto a za chuma. Pa chifukwa chimenechi zinandipangitsa kusakasaka ntchito mwa amwenye. Ndalama zomwe ndimapeza kuntchitoko ndimathandizila ana pakhomo, Kulipira fees ya anawa komanso kupangila business. Pakanali pano ntchito yomwe ndimagwira inatha komanso business yanga siyikuyenda. Ndingapange bwanji poti ndinakakonda anawa anakapitiliza sukulu koma ine ndilibe zondiyenereza. Ndithandizeni.